Hoseya 13:14-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndidzawaombola ku, mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako iri kuti? manda, cionongeko cako ciri kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.

15. Cinkana abala mwa abale ace, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kucokera kucipululu; ndi gwero lace lidzaphwa, ndi kasupe wace adzauma, adzafunkha cuma ca akatundu onse ofunika.

16. Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wace; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.

Hoseya 13