Hoseya 11:4-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za cikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira cakudya.

5. Iye sadzabwerera kumka ku dziko la Aigupto, koma Asuri adzakhala mfumu yace, popeza anakana kubwera.

6. Ndi lupanga lidzagwera midzi yace, lidzatha mipiringidzo yace, ndi kuononga cifukwa ca uphungu wao.

Hoseya 11