1. Pamene Israyeli anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali m'Aigupto.
2. Monga anawaitana, momwemo anawacokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.
3. Koma Ine ndinaphunzitsa Efraimu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwa kuti ndinawaciritsa.