Habakuku 3:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje?Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi,Kapena ukali wanu panyanja,Kuti munayenda pa akavalo anu,Pa magareta anu a cipulumutso?

9. Munapombosola uta wanu;Malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona.Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.

10. Mapiri anakuonani, namva zawawa;Cigumula ca madzi cinapita;Madzi akuya anamveketsa mau ace,Nakweza manja ace m'mwamba.

11. Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;Pa kuunika kwa mibvi yanu popita iyo.Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.

12. Munaponda dziko ndi kulunda,Munapuntha amitundu ndi mkwiyo.

13. Munaturukira cipulumutso ca anthu anu,Cipulumutso ca odzozedwa anu;Munakantha mutu wa nyumba yawoipa,Ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.

14. Munapyoza ndi maluti ace mutu wa ankhondo ace;Anadza ngati kabvumvulu kundimwaza;Kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mabisika.

Habakuku 3