Genesis 9:24-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwace, nadziwa cimene anamcitira iye mwana wace wamng'ono.

25. Ndipo anati,Wotembereredwa ndi Kanani:Adzakhala kwa abale ace kapolo wa akapolo:

26. Ndipo anati:Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu;Kanani akhale kapolo wace.

27. Mulungu akuze Yafeti,Akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wace.

Genesis 9