11. Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo; Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akuru a Aaigupto: cifukwa cace dzina la pamenepo linachedwa Abeli-mizraimu, pali tsidya lija la Yordano.
12. Ndipo ana ace amuna anamcitira iye monga anawalamulira iwo;
13. cifukwa kuti ana ace amuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pace, kwa Efroni Mhiti, patsogolo pa Mamre.