18. Ndadikira cipulumutso canu, Yehova.
19. Ndi Gadi, acifwamba adzampsinja iye;Koma iye adzapsinja pa citende cao.
20. Ndi Aseri, cakudya cace ndico mafuta,Ndipo adzapereka zolongosoka zacifumu.
21. Nafitali ndi nswala yomasuka;Apatsa mau abwino.
22. Yosefe ndi nthambi yobala,Nthambi yobala pambali pa kasupe;Nthambi zace ziyangayanga palinga.
23. Eni uta anabvutitsa iye kwambiri,Namponyera iye, namzunza:
24. Koma uta wace unakhala wamphamvu,Ndi mikono ya manja ace inalimbitsidwaNdi manja a Wamphamvu wa Yakobo.(Kucokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israyeli,)
25. Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iweNdi madalitso a Kumwamba,Madalitso a madzi akuya akukhala pansi,Madalitso a mabere, ndi a mimba.
26. Madalitso a atate wakoApambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,Kufikira ku malekezero a patari a mapiri a cikhalire;Adzakhala pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ace.