Genesis 46:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndi ana amuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Yabi, ndi Simroni.

14. Ndi ana amuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaledi.

15. Amenewo ndi ana amuna a Leya, amene anambalira Yakobo m'Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wace Dina; ana amuna ndi akazi onse: ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.

16. Ndi ana amuna a Gadi: Zifioni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Ezboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.

17. Ndi ana amuna a Aseri: Yimna, ndi Yisiva, ndi Yisivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Maliki eli.

18. Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wace wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi.

Genesis 46