21. Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.
22. Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wace; pakuti akamsiya atate wace, atate wace adzafa.
23. Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga,
24. Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanus atate, wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga.
25. Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife cakudya pang'ono.