Genesis 43:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?

8. Ndipo Yuda anati kwa atate wace Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.

9. Ine ndidzakhala cikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, cifukwa cace cidzakhala pa ine masiku onse:

10. pakuti tikadaleka kucedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.

11. Ndipo Israyeli atate wao anati kwa iwo, Ngati comweco tsopano citani ici: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta a mankhwala pang'ono, ndi uci pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;

12. nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanacita dala;

13. mutengenso mphwanu, nimuoyamuke, mupitenso kwa munthu uja:

14. Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu cifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.

Genesis 43