7. Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?
8. Ndipo Yuda anati kwa atate wace Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.
9. Ine ndidzakhala cikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, cifukwa cace cidzakhala pa ine masiku onse:
10. pakuti tikadaleka kucedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.
11. Ndipo Israyeli atate wao anati kwa iwo, Ngati comweco tsopano citani ici: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta a mankhwala pang'ono, ndi uci pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;
12. nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanacita dala;
13. mutengenso mphwanu, nimuoyamuke, mupitenso kwa munthu uja: