Genesis 42:29-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;

30. kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankharwe, natiyesa ife ozonda dziko.

31. Koma ife tinati kwa iye, Tiru anthu oona; sitiri ozonda;

32. tiri abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani.

33. Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;

34. idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: comweco ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzacita malonda m'dziko muno.

35. Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lace; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa,

Genesis 42