37. Ndipo cinthuco cinali cabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ace.
38. Ndipo Farao anati kwa anyamata ace, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwace?
39. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.
40. Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wacifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.