Genesis 41:13-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudacitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampacika.

14. Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamturutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, napindula malaya ace, nalowa kwa Farao.

15. Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.

16. Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.

17. Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa nyanja;

18. ndipo taona, zinaturuka m'nyanjamo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango;

19. ndipo, taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinaturuka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Aigupto;

20. ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa,

21. Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba.

22. Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino;

23. ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao;

24. ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine.

Genesis 41