16. Ndipo Kaini anaturuka pamaso pa Yehova, ndipo anakhalam'dziko la Nodi, kum'mawa kwace kwa Edene.
17. Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.
18. Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke.
19. Ndipo Lameke anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lace la wina ndi Ada, dzina lace la mnzace ndi Zila.
20. Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe,
21. Ndi dzina la mphwace ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oyimba zeze ndi citoliro.