Genesis 35:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Beteli nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.

2. Ndipo Yakobo anati kwa a banja lace, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Cotsani milungu yacilendo iri mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zobvala zanu:

Genesis 35