Genesis 30:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wace akhale mkazi wace; ndipo Yakobo analowa kwa iye.

5. Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.

6. Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; cifukwa cace anamucha dzina lace Dani.

7. Ndipo Biliha mdzakazi wace wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna waciwiri.

8. Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkuru wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamucha dzina lace Nafitali.

9. Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wace, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wace.

10. Ndipo Zilipa mdzakazi wace wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna.

Genesis 30