Genesis 25:8-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m'ukalamba wace wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wace.

9. Ndipo ana ace Isake ndi Ismayeli anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efroni mwana wace wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre;

10. munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wace.

11. Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wace; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi.

12. Mibadwo ya Ismayeli mwana wamwamuna wace wa Abrahamu, amene Hagara M-aigupto mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:

13. ndipo maina a ana a Ismayeli, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismayeli ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Abideele, ndi Mibisamu,

14. ndi Misima, ndi Duma; ndi Masa;

15. ndi Hadada, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema;

16. ana a Ismayeli ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akaronga khumi ndi awiri m'mitundu yao.

17. Zaka za moyo wa Ismayeli ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wace.

18. Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwace kwa Aigupto, pakunka ku Asuri: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ace onse.

19. Mibadwo ya Isake mwana wace wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isake:

20. ndipo Isake anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Msuriya wa ku Padanaramu, mlongo wace wa Labani Msuriya.

Genesis 25