7. Masiku a zaka za moyo wace wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.
8. Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m'ukalamba wace wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wace.
9. Ndipo ana ace Isake ndi Ismayeli anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efroni mwana wace wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre;
10. munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wace.
11. Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wace; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi.
12. Mibadwo ya Ismayeli mwana wamwamuna wace wa Abrahamu, amene Hagara M-aigupto mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi: