18. m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lap ansi idzadalitsidwa: cifukwa wamvera mau anga.
19. Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ace, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.
20. Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana;
21. Huzi woyamba ndi Buzi mphwace, ndi Kemueli atate wace wa Aramu;
22. ndi Kesede, ndi Hazo, ndi Pilidasi ndi Yidilafi, ndi Betuele.
23. Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwace wa Abrahamu.