5. Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; cifukwa Yehova Mulungu sanabvumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;
6. kama inakwera nkhungu yoturuka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka.
7. Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwace; munthuyo nakhala wamoyo.