10. Ndipo unaturuka m'Edene mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nucita miyendo inai.
11. Dzina la wakuyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golidi;
12. golidi wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu.
13. Dzina la mtsinje waciwiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi.
14. Dzina la mtsinje wacitatu ndi Hidikeli: umenewo ndiwo wakuyenda ca kum'mawa kwace kwa Asuri. Mtsinje wacinai ndi Pirate.
15. Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Eriene kuti aulime nauyang'anire.
16. Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko;