Genesis 17:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.

2. Ndipo ndidzapangana pangano langa ndi Ine ndi iwe, ndipo ndidzacurukitsa iwe kwambiri.

Genesis 17