Genesis 12:18-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nciani ici wandicitira ine? cifukwa canji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako?

19. Cifukwa canji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nucoke.

20. Ndipo Farao analamulira anthu ace za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wace ndi zonse anali nazo.

Genesis 12