11. amene kale sanakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;
12. amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weni weni wa ine.
13. Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino:
14. koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafuna kucita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.
15. Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi cifukwa ca ici, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse;
16. osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.