Ezekieli 9:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe cizindikilo pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira cifukwa ca zonyansa zonse zicitidwa pakati pace.

5. Nati kwa enawo, nditikumva ine, Pitani pakati pa mudzi kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musacite cifundo;

6. iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu ali yense ali naco cizindikilo, ndipo muyambe pa malo anga opatulika, Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.

7. Nati kwa iwo, Muipse nyumbayi ndi kudzaza mabwalo ndi ophedwa, mukani. Ndipo anaturuka, nakantha m'mudzimo.

8. Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kupfuula, ndi kuti, Kalanga ine. Ambuye Mulungu! kodi mudzaononga otsala onse a Israyeli pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?

Ezekieli 9