1. Pamenepo Iye anapfuula m'makutu mwanga ndi mau akuru, ndi kuti, Asendere oyang'anira mudzi, ali yense ndi cida cace coonongera m'dzanja lace.
2. Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya cipata ca kumtunda coloza kumpoto, ali yense ndi cida cace cophera m'dzanja lace; ndi munthu mmodzi pakati pao wobvala bafuta, ndi zolembera nazo m'cuuno mwace. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.