Ezekieli 48:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo m'mwemo mudzakhala copereka copatulika ca ansembe kumpoto, zikwi makumi awiri mphambu zisanu a m'litali mwace, ndi kumadzulo zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kum'mawa zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kumwela zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace; ndi pakati pace pakhale malo opatulika a Yehova.

11. Cidzakhala ca ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israyeli, ndi muja anasokera Alevi.

12. Ndi ciperekoco cikhale cao cotapa pa copereka ca dziko, ndico copatulikitsa pa malire a Alevi.

13. Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace; m'litali mwace monse ndimo zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwace zikwi khumi.

14. Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti liri lopatulika la Yehova.

15. Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwace, cakuno ca zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za nchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pace.

16. Ndi miyeso yace ndi iyi: mbali ya kumpoto, mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwela, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kummawa, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, zikwi zinai mphambu mazana asanu.

Ezekieli 48