4. Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'maondo. Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'cuuno.
5. Atatero anayesanso cikwi cimodzi, ndipo mtsinje wosakhoza kuoloka ine, popeza madzi adakula, madzi osambira, mtsinje wosaoloka munthu.
6. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, waona ici? Nanditenga kundikwezetsa ndi mtsinje.
7. Nditabwera tsono, taonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri tsidya lino ndi lija.
8. Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa aturukira ku dera la kum'mawa, natsikira kucidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ace.