Ezekieli 44:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira nchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga ziri zonse zopatulikitsazo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazicita.

14. Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa kacisi kwa utumiki wace wonse, ndi zonse zakumacitika m'mwemo.

15. Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israyeli, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;

16. iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira ku gome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.

17. Ndipo kudzatero, polowa iwo ku zipata za bwalo lam'kati abvale zobvala zabafuta; koma zaubweya asazibvale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi m'kacisi.

18. Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'cuuno mwao; asabvale m'cuuno kanthu kali konse kakucititsa thukuta.

Ezekieli 44