19. Upatse ansembe Alevi, a mbeu ya Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwana wa ng'ombe, akhale wa nsembe yaucimo.
20. Nutengeko mwazi wace, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pa ngondya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wace pozungulira; motero uliyeretse ndi kulicitira cotetezera.
21. Utengenso ng'ombe ya nsembe yaucimo, aipsereze pa malo oikika a kacisi kunja kwa malo opatulika.
22. Ndipo tsiku laciwiri upereke tonde wopanda cirema, akhale nsembe yaucimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.