Ezekieli 39:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe ucoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe ku mapiri a Israyeli;

3. ndipo ndidzakantha uta wako kuucotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mibvi yako ku dzanja lako lamanja.

4. Udzagwa pa mapiri a Israyeli, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zirombo za kuthengo, akuyese cakudya.

5. Udzagwa kuthengo koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.

Ezekieli 39