5. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu lonse, amene anadzipatsira dziko langa likhale colowa cao ndi cimwemwe ca mtima wonse, ndi, mtima wopeputsa, kuti alande zace zonse zikhale zofunkha.
6. Cifukwa cace unenere za dziko la Israyeli, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;
7. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao.
8. Koma inu, mapiri a Israyeli, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israyeli zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika.
9. Pakuti taonani, Ine ndikhalira nanu kumodzi, ndipo ndidzakutembenukirani; ndipo mudzabzalidwa ndi kupaliridwa,
10. ndipo ndidzakucurukitsirani anthu nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi, ndi m'midzimo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa midzi.
11. Ndipo ndidzakucurukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzacuruka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzacitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
12. Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israyeli; adzakhala nawe dziko lao lao, ndipo udzakhala colowa cao osafetsanso ana ao.
13. Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;
14. cifukwa cace sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso amtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.
15. Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzaseozanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.
16. Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,
17. Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israyeli anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi macitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga cidetso ca mkazi wooloka.
18. M'mwemo ndinawatsanulira ukali wanga, cifukwa ca mwazi anautsanulira padziko, ndi cifukwa ca mafano analidetsa dziko nao;
19. ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa macitidwe ao ndinawaweruza.
20. Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, naturuka m'dziko mwace.