13. Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;
14. cifukwa cace sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso amtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.
15. Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzaseozanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.
16. Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,
17. Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israyeli anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi macitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga cidetso ca mkazi wooloka.