Ezekieli 34:3-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Mukudya mafuta, mubvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa.

4. Zofoka simunazilimbitsa; yodwala simunaiciritsa, yotyoka simunailukira chika, yopitikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa,

5. M'mwemo zinamwazika posowa mbusa, nizinakhala cakudya ca zirombo ziri zonse za kuthengo, popeza zinamwazika.

6. Nkhosa zanga zinasokera ku mapiri ali onse, ndi pa citunda ciri conse cacitali; inde nkhosa zanga zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.

Ezekieli 34