Ezekieli 30:4-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndi lupanga lidzadzera Aigupto, ndi m'Kusi mudzakhala kuwawa kwakukuru, pakugwa ophedwa m'Aigupto; ndipo adzacotsa aunyinji ace, ndi maziko ace adzagadamuka,

5. Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Kubi, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.

6. Atero Yehova, Iwonso ocirikiza Aigupto adzagwa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatsika, kuyambira nsanja ya Sevene adzagwa m'kati mwace ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

Ezekieli 30