Ezekieli 29:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aaigupto ku mitundu ya anthu kumene anamwazikirako;

14. ndipo ndidzabweza undende wa Aigupto, ndi kuwabwezera ku dziko la Patro, ku dziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka,

15. Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawacepsa, kuti asacitenso ufumu pa amitundu.

16. Ndipo sudzakhalanso cotama ca nyumba ya Israyeli, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

17. Ndipo kunali caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

18. Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anacititsa ankhondo ace nchito yaikuru yoponyana ndi Turo; mitu yonse inacita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Turo, iye kapena ankhondo ace, pa nchito anagwirayo;

19. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Aigupto kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzacoka nao aunyinji ace, nadzafunkha ndi kulanda zace, ndizo mphotho ya khamu lace.

20. Ndamninkha dziko la Aigupto combwezera nchito yace, popeza anandigwirira nchito, ati Ambuye Yehova.

Ezekieli 29