Ezekieli 28:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu;

7. cifukwa cace taona, ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.

8. Adzakutsitsira kumanda, nudzafa mafedwe a ophedwa m'kati mwa nyanja.

9. Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.

10. Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.

11. Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

Ezekieli 28