3. taona, ndiwe wanzeru woposa Danieli, palibe cinsinsi angakubisire;
4. mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera cuma, wadzionereranso golidi ndi siliva mwa cuma cako;
5. mwa nzeru zako zazikuru ndi kugulana malonda kwako wacurukitsa cuma cako, ndi mtima wako wadzikuza cifukwa ca cuma cako;
6. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu;
7. cifukwa cace taona, ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.