Ezekieli 27:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Aigupto, likhale ngati mbendera yako; cophimba cako ndico nsaru yamadzi ndi yofiirira zocokera ku zisumbu za Elisa.

8. Okhala m'Zidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Turo, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako.

9. Akr-ru a ku Gebala ndi eni luso ace anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amarinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.

10. Aperisiya, Aludi, Apuri, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapacika cikopa ndi cisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.

11. Anthu a Ativadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapacika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.

Ezekieli 27