Ezekieli 27:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Tarisi anagulana nawe malonda m'kucuruka kwa cuma ciri conse; anagula malonda ako ndi siliva ndi citsulo, seta ndi ntobvu.

13. Yavani, Tuba, Meseke, anagulana nawe malonda; ndi anthu amoyo ndi zotengera zamkuwa anagulana nawe malonda.

14. Iwo a nyumba ya Togarima anagula malonda ako ndi akavalo, ndi akavalo a nkhondo, ndi nyuru.

15. Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda.

16. Aramu anacita nawe malonda cifukwa ca zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsaru yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.

Ezekieli 27