18. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
19. Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babulo; zonse ziwiri zicokere dziko lomwelo; nulembe cizindikilo colozera, ucilembe pa mphambano ya njira ya kumudzi.
20. Uiike njira yodzera lupanga kumka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.
21. Pakuti mfumu ya ku Babulo aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mibvi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi ciwindi.