1. Ndipo iwe, takwezera akalonga a Israyeli nyimbo ya maliro,
2. uziti, Mai wako ndi ciani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ace pakati pa misona.
3. Ndipo unalera mmodzi wa ana ace, iye nasanduka msona, unaphunzira kugwira nyama, unalusira anthu.