Ezekieli 18:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anandidzera mau a Yehoya, akuti,

2. Mutani inu ndi kunena mwambi uwu za dziko la Israyeli, wakuti, Atate adadya mphesa zosacha, ndi mano a ana ayayamira.

3. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, simudzaonanso cifukwa ca kunena mwambiwu m'Israyeli.

4. Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wocimwawo ndiwo udzafa.

5. Koma munthu akakhala wolungama, nakacita ciweruzo ndi cilungamo,

6. wosadya pamapiripo, wosakweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,

Ezekieli 18