Ezekieli 17:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Farao ndi nkhondo yace yaikuru, ndi khamu lace launyinji, sadzacita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.

18. Pakuti anapepula lumbiro, ndi kutyola pangano, angakhale anapereka dzanja lace; popeza anacita izi zonse sadzapulumuka.

19. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analityola, ndidzawabweza pamutu pace.

20. Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babulo, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwace anandilakwira nako.

Ezekieli 17