Ezekieli 16:53-60 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

53. Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ace, ndi undende wa Samariya ndi ana ace, ndi undede wa andende ako pakati pao;

54. kuti usenze manyazi ako, ndi kuti ucite manyazi cifukwa ca zonse unazicita pakuwatonthoza.

55. Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ace adzabwerera umo unakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale.

56. Ndipo sunakamba za mbale wako Sodomu pakamwa pako tsiku la kudzikuza kwako;

57. cisanabvundukuke coipa cako monga nthawi ya citonzo ca ana akazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana akazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.

58. Wasenza coipa cako ndi zonyansa zako, ati Yehova.

59. Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzacita ndi iwe monga umo unacitira; popeza wapepula lumbiro ndi kutyola pangano.

60. Koma ndidzakumbukila Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.

Ezekieli 16