Ezekieli 16:47-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Koma sunayenda m'njira zao, kapena kucita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kubvunda kwako, m'njira zako zonse.

48. Pali ine, ati Ambuye Yehova, Sodomu mng'ono wako sanacita, iye kapena ana ace akazi, monga umo unacitira iwe ndi ana ako akazi.

49. Taona, mphulupulu ya mng'onowako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kucuruka kwa cakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ace; ndipo sanalimbitsa dzanja la wosauka ndi wosowa.

50. Ndipo anadzikuza, nacita conyansa pamaso panga; cifukwa cace ndinawacotsa pakuciona.

51. Ngakhale Samariya sanacita theka la zocimwa zako, koma unacurukitsa zonyansa zako kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazicita.

Ezekieli 16