1. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2. Wobadwa ndi munthu iwe, Dziwitsa Yerusalemu zonyansa zace, nuziti,
3. Atero Ambuye Yehova kwa Yerusalemu, Ciyambi cako ndi kubadwa kwako ndiko ku dziko la Akanani; atate wako anali M-amori, ndi mai wako Mhiti.
4. Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadula ncofu yako, sanakuyeretsa ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthira mcere konse, kapena kukukulunga m'nsaru ai.
5. Panalibe diso linakucitira cifundo, kukucitira cimodzi conse ca izi, kucitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwake,