9. Ndipo akaceteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamceta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israyeli.
10. Ndipo adzasenza mphulupulu yao, mphulupulu ya mneneri idzanga mphulupulu ya uja wamfunsira;
11. kuti nyumba ya Israyeli isasocerenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.