1. Ndipo mau a Yehova anandidzera ine, akuti,
2. Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israyeli onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwao mwao, Tamverani mau a Yehova.
3. Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu wao wao, cinkana sanaona kanthu.
4. Aneneri ako, Israyeli, akhala ngati nkhandwe m'mapululu.
5. Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israyeli, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.